ZOTSATIRA ZA ZOKAMBIRANA ZOKHUDZA MA YOUTH CAMPS KU MPOTO
DATE: 19 JANUARY 2013
Pemphero lotsekulira: Deacon Luwanda (Dunduzu)
Kupereka mbiri ya
zokambirana zakale. (recap)
Malingana ndikuti ma secretary onse awiri sanabwere ku
zokambiranazi wapampando wa komitiyi Frighton Kachule ndi amene anapereka
mbiriyi m`malo mwake. Cholinga cha mbiri chinali kukumbutsana zomwe
anakambirana kale, komanso kufuna kudziwa zomwe zinakwaniritsidwa ndi zomwe
zikufunika kuchitika.
Mbiri ya
zachuma
Atatha chairman kupereka lipotili naye msungichuma anapereka
lipoti lake la za chuma: Iye mu lipoti lake anati ndalama zonse zinali 4000
kwacha koma pamene tinakumana pa tsikuli tinagwiritsa tchito ndalama zokwana 1.160
kwacha zomwe tinagulira chakudya ndipo pakali pano kuthumba kwathu kwatsala
ndalama zokwana 2,840 kwacha. Ndalamazi sizikukwana kuyendetsera bungwe la
chinyamata pa regional level kotero chinyamata chathu chikuyenera kupeza njira
zomwe zingathandize kukweza chuma chathu. (fumbi ndiwe mwini)
Mfundo zomwe
zinakambidwa:
- Kalata yochokera ku Luwazi joint
- Malo eni eni ochitirapo half ndi full camp
- Kukonza masiku a ma youth camps
- Camp fee
- Kukonza dongosolo la kasonkhedwe ka zakudya za pa half camp
- Malamulo apa camp
- Mbiri (report) yochokera ku National Youth Committee
MUTU OYAMBA:
KALATA YOCHOKERA KU LUWAZI JOINT
Itafika nthawi yolandira nfundo
zoti tikambirane kuchokera kwa nthumwi za komiti, Luwazi joint kudzera mwa
chairman wawo Charles Mkandawire inapereka kalata yawo yomwe inali yodandaula
kuti iwo akufuna full camp osati half camp monga momwe zinakhalira. Ndipo chairman
wakomitiyi Frighton Kachule anawerenga kalatayo pamanso pa anthu onse yomwe inali
motere:
Luwazi Y Joint
Prvate Bag 63
Mzuzu
5th January 2013
The chairman
Northern Youth
Association Committee
Mzuzu
Mutu: Kalata wokhudza youth camp
Takhala pansi
ndikugwirizana kuti ife tikupempha full camp osati half camp pa zifukwa izi:
i.
Ife kuno takhalitsa osakhala ndi
full camp
ii. Ife timaziwa kuti timayendera
circle pokonza camp osati chisawawa
iii. Ifeyo tayenda kwambiri kwa
anzathu
Ngati zingalephere
kutipatsa full camp ndiye tikupempha kuti ndibwino kuti nayo half camp yomwe
munatipatsa ipite kaye kwa ena, kaamba koti ifeyo sitili okonzeka kukhala ndi
half camp ndipo tidzadikira mpaka chaka chomwe mudzatipatsire full camp. Komabe
izi sizikusonyeza kuti tiri okhumudwa ayi, ife tili okonzeka kupita kulikonse
komwe kungakhale camp.
M`malo mwa komiti
yonse ya Luwazi Youth Joint, ine wanu mwa mbuye:
Michael
Mtepa Charles
Mkandawire
(Secretary) (Chairman )
Pakukambirana za nkhaniyi, komiti inawona kuti kunali
kofunika kuwathandiza pa pempho lawo pa zifukwa zomwe anenazo komanso panali zifukwa
zina zowonjezera pamenepa monga:
·
Pali
chikayiko ngati a Lusimbo angakwanitse kukonzekera full camp
·
Nthawi
zambiri achinyamata aku Lusimbo sawonetsa chidwi cheni cheni pakusonkhana ndi
anzawo.
· Malo
komanso zinthu zokonzekera msonkhano ndizosadalirika ku Lusimbo kufikira akulu
akulu association atayenderako kaye
Pazifukwa zonsezi, pomaliza komiti inagwirizana kuti tsopano Half camp ipite ku Lusimbo ndipo Full camp
ipite ku Luwazi
Koma komitiyi inatsutsa nfundo nambala 2 ya mkalata wa
Luwazi yomwe imanena kuti iwo amadziwa
kuti pokonza misonkhano ya camp zimayendera circle osati chisawawa. Pamenpa
chairman anafotokoza kuti 1). Ganizo loyika msonkhano umodzi ku Henga joint
linabwera pofuna kuwaganizira achinyamata a Henga joint pankhani ya transport
kuti asayende ma ulendo awiri atali atali okha okha chaka chino chokha
malingana ndi kukwera mitengo ya ma transport. 2). Ndizoona kuti mwadongosolo camp ina imayenera
ku chitira ku Mzuzu koma Kaamba koti a Mzuzu joint akhala otanganidwa ndi
msonkhano wa ukulu wa zimayi chaka chino ndiye kukhala kovuta kuti
akonzekerenso camp. Ndichifukwa chake zawoneka ngati kuti sitinayendere circle
posankha malo ochitira ma-camp.
Langizo kwa onse:
Komabe ndi bwino kuti tisamakhale ndi chizolowezi chakuti
zinthu zimayenda chonchi ayi, zinthu zimasintha malingana ndi nyengo yake.
Tisamayiwale kuti chizolowezi nthawi zonse chimawononga zinthu.
Phunziro lomwe tingapeze mu
nkhaniyi:
Tikuyamikira kwambiri njira
imene Luwazi joint inagwiritsa tchito pofuna kuthetsa vuto lomwe analiwona.
Njirayi ikupereka ulemu kwa komityi ndi
nthumwi zonse pozindikira kuti amataya ndalama komanso nthawi pofuna
kuti akambirane zinthu ngati zimenezi ndi chifukwa chake sanafune kuti
zingothera pafoni kapena kumangoveketsa nkhani zamabodza zomwe sindizo.
Ndibwino kuti titengerepo phunziro kuti ngati pali nkhani yomwe
sinakusangalatseni kapena mwafuna kuti pena pake pa sinthidwe ndibwino kulemba
kalata kapena kutumiza nthumwi yanu ku zokambirana za association kuti nkhaniyo
ikakambidwe pa komiti osati kumangoyamba kufalitsa mabodza kapena pafoni ayi.
Zindikirani kuti a Luwazi joint sanachiyesere chamwayi kuti poti chairman ndi
wa ku joint kwawo ndiye angopanga zomwe akufuna ayi komanso naye chairman
sanatengere kuti poti ndi anthu a joint yake ndiye angosintha zinthu popanda
kudzera kukomiti ayi. Dziwani kuti chairman siwa joint imodzi ayi ndipo
sayimira mbali ayi. Tiyeni tiziyendetsa zinthu mudongosolo kuti chinyamata
chathu chikhale chopambana.
MUTU WA CHIWIRI:
MALO ENI ENI OCHITIRA MISONKHANO YA CAMP
Malo ochitira misonkhano ya
youth camp ndi Lusimbo yomwe ndi Henga joint ndi Luwazi komwenso ndi Luwazi joint. Malingana
ndi zokambirana za pa 24 Novermber 2012 komiti inawunika zina mwa fundo zomwe
zimapangitsa kuti kafalitsidwe ka uthenga wabwino kasapite pa tsogolo mu mpingo
mwathu komwe tinapeza kuti kuphatikiza kuti tilibe njira zamphanvu zofalitsara
uthenga wa Mulungu, tikamachita misonkhano yathu timachitira malo amodzi modzi chaka
ndi chaka monga pa tchalitchi zomwe zimapangitsa kuti tisamafikire anthu omwe
akusowekera uthengawu. Pa chifukwa cha ichi komiti inagwirizana kuti tsopano
tiyense kumapangira misonkhano ya youth
camp kutali ndi ma tchalitchi, ndicholinga choti tikafikirenso anthu ena
achilendo komanso ngati njiri imodzi yofalitsira mbiri ya mpingo wathu kuti uzidziwika
ku madera ambiri adziko lino. Kotero tinawapempha ma joint onse amene kukachitikire
camp kuti akafune malowa kutali ndi ma tchalitchi awo:
Ku Lusimbo, Half camp ikuyenera kukachitikira pa Chichi primary school pamene ku Luwazi full camp ikuyenera kudzachitikira pa Mwambazi primary school koma ngati pangakhale kusintha
tidzadziwitsidwa nthawi ya camp isanafike:
Malo a Half Camp 2013
Henga Joint (Rumphi) > Lusimbo SDB Church > Chichi Primary School
Luwazi Joint (Nkhata Bay) > Luwazi SDB
Church > Mwambazi Primary School
MUTU WACHITATU:
KUKONZA MASIKU OCHITIRA MISONKHANO YA YOUTH
CAMP
Half
camp
APRIL 2013
S M T W T F S
1 2 3 4 5 6
7 8 9 {10 11 12 13}
14 15 16 17 18 19 20
21 22 23 24 25 26 27
28 29 30
|
Idzayamba pa Wednesday, 10 April mpaka pa Saturday (Sabbath) 13 April 2013 (masiku atatu)
Full
camp
|
Idzayamba pa Sunday, 11 August mpaka pa Saturday (Sabbath) 17 August 2013 (masiku 7)
Masikuwa anakonzedwa malingana ndi kalindala ya ma sukulu onse
dziko muno yomwe ili motere
Term
|
Tsiku lotsekulira
|
Tsiku lotsekera
|
Utali wa nyengo ya Masiku a
tchuthi
|
Masabata a tchuthi
|
Yoyamba
|
3
March 2012
|
7
December 2012
|
7
December 2013 mpaka pa 6 January 2013
|
Anayi
(4 weeks)
|
Yachiwiri
|
7
January 2013
|
22
March 2013
|
22
March mpaka pa 21 April 2013
|
Anayi (4 weeks)
|
Yachitatu
|
22
April 2013
|
26
July 2013
|
26 July mpaka pa 1 September 2013
|
Asanu (5 weeks)
|
MUTU WACHINAYI:
CAMP FEE
Fundoyi inaperekedwa ndicholinga
chofuna kuwunikanso zaubwino omasonkha camp fee komanso kuyipa kwake ngati
kulipo. Ngakhale kuti ndi chachilendo mu mbiri ya chinyamata kuno ku mpoto ndi
kutinso anthu sanazolowere kusonkha camp fee Komabe anthu ambiri akuyamikira
kuti camp fee ikumathandiza kwambiri maka maka pamene tili pa camp, chitsanzo
camp imene tinali nayo ku Echizweni, malingana ndi kuchepa kwa zakudya
msonkhano unayenera kuthera panjira koma camp fee inatithandiza kugula zakudya
mpaka tinamaliza msonkhano kuphatikiza pamenepa timagulira mankhwala omwe
amatithandizanso kwambiri pa nthawi yomwe tili pamsonkhano. Pachifukwa cha ichi
panali ganizo loti mwina achinyamata asiye kumasonkha zakudya popita ku camp
m`malo mwake tingokweza camp fee, mu m`kukambirana mthumwi zinawona kuti
sikwabwino kuti tingokwezeratu camp fee ndi kuchotsa zakudya zomwe achinyamata
amanyamula kaamba koti kudyamula kwa zakudya kumathandiza kuchepetsa ndalama
zomwe anyamata amawononga pokonzekera youth camp komanso kukweza kwa camp fee kudzapangitsa
kuti anthu ena ovutika komanso achichepere alephere kupita ku camp. Komabe malingana ndi kukwera kwa mitengo ya
zinthu m`dziko muno K250 yomwe timasonkha ngati camp fee sikukwanira ayi kotero
tinagwiri zana kuti camp fee tsopano ikhale K500 aliyense koma tachotsako zakudya zina zomwe timanyamula monga:
zomwela tea, mafuta ophikira, mchere, masamba a tea ndi sugar, m`malo mwake
achinymata azingonyamula ufa ndi ndiwo basi
>>Camp fee: K500 Aliyense
♣
Akulu akulu
(am`khala pakati) komanso aziphunzitsi onse akuyenera kudzanyamula camp fee
pobwera ku camp, koma sakuyenera kusonkha nawo zakudya komaso transport
ikuyenera kukonzedwa ndi achinyamata omwe akuyenda nawo.
MUTU WACHISANU:
DONGOSOLO LA KASONKHEDWE KA
ZAKUDYA ZA HALF CAMP
Henga Joint
|
Tikuyembekezera Anthu
osachepera
|
Ufa
|
Ndiwo / Ndalama
|
Khanga
+ Phompha
|
15
|
Mathini Atatu (3)
|
10
kg Nyemba kapena ndalama K2000
|
Mzale
|
30
|
Ma thini 6
|
20 kg Nyemba kapena ndalama K4000
|
Lusimbo
|
15
|
Mathini Atatu (3)
|
10
kg Nyemba kapena ndalama K2000
|
Uzumala
+ Sasi
|
10
|
Mathini awiri
(2)
|
10
kg Nyemba kapena
ndalama K 1500
|
Luwazi Joint
|
Tikuyembekezera Anthu
osachepera
|
Ufa
|
Ndiwo / Ndalama
|
Majiga
+ Chinguluwe
|
3
|
Thini Lomodzi (1)
|
5
kg Nyemba kapena ndalama K1000
|
Lisale
+ Manyenyezi
|
15
|
Mathini Anayi (3)
|
10 kg Nyemba kapena ndalama K2000
|
Luwazi
|
20
|
Mathini Atatu ( 4)
|
15
kg Nyemba kapena ndalama K3000
|
Mzuzu Joint
|
Tikuyembekezera Anthu
osachepera
|
Ufa
|
Ndiwo / Ndalama
|
Dunduzu
|
30
|
Ma thini 6
|
20 kg Nyemba kapena ndalama K4000
|
Jandalala
|
12
|
Mathini awiri
( 2)
|
10
kg Nyemba kapena ndalama K2000
|
Mchengautuwa
|
10
|
Mathini Atatu (2)
|
10
kg Nyemba kapena ndalama K1500
|
Zolozolo
|
10
|
Mathini awiri
(2)
|
10
kg
Nyemba kapena ndalama K1500
|
Zindikirani kuti pa anthu
asanu aliwonse pakuyenera pakhale thini
limodzi la ufa komanso 5kg nyemba kotero chiwerengero chikakwera ndi anthu 5
aliwonse mukuyeneranso kuwonjezera kuchuluka kwa chakudya chanu malingana ndi
mulingo omwe waikidwawu. Kumbukiraninso kuti dongosolo la chakudya ichi ndi
la pa Half camp basi, ya full camp ikonzedwabe kutsogolo kuno.
MUTU WACHISANU
NCHIMODZI:
MALAMULO APA CAMP
Pofuna kuchepetsa zibwana zomwe
zimachitika ku camp, komiti inawona kuti ndikofunikira kuti pakhale malamulo
omwe aliyense wopita ku camp akuyenera kuwatsatira. Ndipo malamulo amenewa
akuyenera kugwira ntchito kwa wina aliyense posatengera komwe akuchokera,
maonekedwe, kukula kapenanso udindo omwe alinawo. Ndipo ndi cholinga cha
komitiyi kudziwitsiratu achimata komanso anthu onse ofuna kudzakhala nawo pa ma
camp anthu kuti adziwiretu malamulo amenewa ndipo yense obwera ku camp
kusonyeza kuti akugwirizana nawo malamulowa ndikuti akuyenera kutsatira zonse.
Ndipo malamulowo ali otere:
YENSE
WOPHWANYA MALAMULO OTSATIRAWA PA CAMP AKUYENERA KUBWEZEDWA
1) Aliyense akuyenera kupezeka pa
camp nthawi iliyonse kuyambira tsiku lofikira mpaka lomaliza
i.
Ngali
ali ndi zochitazina ndi bwino akachite asanafike pa camp kapena itatha camp
2) Aliyense
akuyenera kupezeka pakalasi panthawi ya mphunziro
3) Ikakwana
nthawi yogonera aliyense akuyenera kukagona pamodzi ndi amnzake onse
i.
Pasapezeke
wina palibe pa nthawi yogona kumalo komwe wapatsidwa kugona ndi amnzake
4) Sipadzapezeka
munthu opita kogona thawi isanakwane
i.
Ofuna
kugona pazifukwa zina monga kudwala akuyenera kugona pomwe pali amnzake kapena
pa kalasi pomwepo kufikira nthawi yokagona itakwana
5) Munthu
asayende mopitilira malire omwe ayikidwa pa camp
6) Aliyense
akuyenera kuvala modzilemekeza
i.
Sibwino
kuvala zovala, zothina, zominula, zowonekera mkati, zikuku zikulu (over size)
kukhwefula, ma tcheni, zibangiri, nyotsonyotso ndi zina zambiri.
7) Nthawi
ya chakudya ikhale imodzi, chakudyanso chimodzi
i.
Ndibwino
kuwonetsetsa kuti zipangizo zolandilira zakudya zilipo tikamayandikira
kulandila chakudya
ii.
Pasapezeke
munthu akumachedwa ndi kuchita zina panthawi ya chakudya
8) Asachoke
munthu pa camp ndikuyendera zinthu zina osati za pa camp
i.
Ngati
munthu ali ndi zochita zina, monga, kutumidwa ndi makolo kapena kukawona abale
ndi bwino kuti azichitiratu izi asanafike ku camp kapena itatha camp, chifukwa
zimenezi zimasokoneza chitetezo cha pa camp.
9) Malo
ogona akhale amodzi malingana ndi gulu lomwe munhtu wapatsidwa
i.
Asapezeke
munthu akukagona kunyumba kapena kwina kwake kuleka malo omwe wapatsidwa pa
camp-po
10) Nthawi
yosamba ikhale imodzi
i.
Asapezeke
munthu akupita kukasamba nthawi ya zochitika zina: monga (nthawi ya phunziro
kapena kudya ndibwino kuti awonetsetse ngati akuchita zimenezi asasoneze
zochitika zina)
ii.
Asapezeke
munthu akupita kukasamba kwina kusiya malo omwe wapatsidwa pa camp- po
(chifukwa zimasokoneza dongosolo la kasambidwe komanso limayambitsa
chisokonekero popeza aliyense amakasamba komwe wafuna)
11) Gulu
la chinyamata lililonse lizipita ndi am`khala pakati akulu akulu m`modzi kapena
awiri popita ku camp
i.
Am`khala
pakatiwa akhoza kukhala akulu ampingo ( ma dkioni ) kapena munthu aliyense koma
wamkulu yemwe angathe kulangiza bwino achinyamata.
1.
Akuyeneranso
kukhala amayi womwe angalangize bwino atsikana komanso m`bambo amene
angatsogolere achinyamata bwino.
12) Gulu
lililonse la chinyamata likuyenera kunyamula chakudya chokwanira monga momwe
dongosolo likunenera
i.
Gulu
lomwe lidzanyamule chakudya choperewera likuyenera:
1.
Kulipitsidwa
chindapusa choyelekeza chakudya chomwe chapereweracho kapena
2.
Kubwezedwa
kufikira atakonzeka bwino
Chifukwa kubwera ndi chakudya
choperewere pa camp kumabweretsa mavuto monga:
·
Mapokoso
kwa omwe abweretsa chakudya chokwana komanso
·
Kuperewera
kwa chakudya pa camp zomwe zimazunzitsa anthu osalakwa
·
Kuwonongeka
kwa ndalama zambiri zomwe zikanagwira ntchito zina
MUTU WACHISANU
NCHIWIRI:
MBIRI (REPORT)
YOCHOKERA KU NATIONAL YOUTH COMMITTEE
Chairman
anapereka zotsatira za zokambirana za Malawi youth committee yomwe inachitikira
ku Lilongwe pa 8 December 2012.
Ndipo
zina za izo kunali ku sankhanso komiti yatsopano imene idziyendetsa chinyamata
Malawi yonse ndipo inali motere:
Chairman : Maxwell
Maida (Lilongwe)
V chairman : Malumbo Mkandawire (Blantyre)
Secretary : Hannah
Ganunga (Lilongwe)
V-Secretary : Chancy Mbewe (Thyolo)
Treasure : Peter
Mbite (Thyolo)
Activity Coordinator : Tennis
Molande (Lilongwe)
Committee members
: Billy
Sokole (Mzuzu)
: Frighton
Kachule Nkhata Bay
: Central
Region Chairman (……………..)
: Southern
Region Chairman (………………)
Unform:
National
committee inakhazikitsa uniform yomwe
mtundu wake ndi navy blue pansi ndi white m`mwamba ndipo ma chairman onse a
joint anapatsidwa zitsanzo za msalu zimenzi, ndipo aliyense ofuna kukagula
msaluzi akuyenera kufotokozera chairman kuti amupatse chitsanzo ndi cholinga
choti isakasiyane posankha: Mukafuna kudziwa zambiri funsani a chairman a joint
yanu kuti akufotokozereni bwino kapena mungathe kuimba foni kwa chairman wa
association pa 0888725175. Ndipo munthu akafuna kusoketsa suti, yonse idzikhala
ya navy blue pansi ndi m`mwamba momwe. Msapato
zakuda
Ndipo aliyense akupemphedwa kuti akhale atagula unformyi
potha pa chaka chino
Pemphero lomaliza: Mr
Mbewe (Dunduzu)
Ambuye akhale ndi inu nonse pamene tikukonzekera half camp
imeneyi
M`malo mwa komiti yonse ine wanu mwa mbuye
Frighton Kachule
(Northern youth chairman)
No comments:
Post a Comment